Exodus 28:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Upangenso mphete ziŵiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zam'munsi za chovala chapachifuwa, ku nsonga yake yam'kati, pafupi ndi chovala cha efodi chija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo upange mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pa nsonga zake ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake, m'katimo ku mbali ya kuefodi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo upange mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace, m katimo ku mbali ya kuefodi.