Exodus 28:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Upangenso mphete zina ziŵiri zagolide, ndipo uzilumikize cham'munsi, kutsogolo kwake kwa malamba aŵiri a pa mapewa a efodi, pafupi ndi misoko, pa lamba wolukidwa mwaluso uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Upangenso mphete zina ziwiri zagolide ndipo uzilumikize kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Upangenso mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.