Exodus 28:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'chovala chapachifuwacho uziikamo zinthu zoyera za Chauta zotchedwa Urimu ndi Tumimu, kuti zimenezo zikhale pa chifuwa cha Aroni akamapita kwa Chauta. Motero Aroni akakhala pamaso pa Chauta, nthaŵi zonse adzakhala ndi zomthandiza kuweruza bwino mpingo wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa chapachifuwa cha chiweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula chiweruzo cha ana a Israele pamtima pake pamaso pa Yehova kosalekeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso uyike Urimu ndi Tumimu mu chovala chapachifuwa cha zoweruziracho, kuti zikhale pamtima pa Aaroni. Choncho Aaroniyo adzakhala akutenga nthawi zonse zida zomuthandizira kuweruza ana a Israeli pamene adzafika pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa capacifuwa ca ciweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula ciweruzo ca ana a Israyeli pamtima pace pamaso pa Yehova kosalekeza.