Exodus 28:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakati pake pa mkanjowo usiye chiboo chopisapo mutu. Chiboo chimenechi chikhale chosokerera mwamphamvu mozungulira monse, ngati khosi la malaya, kuti mkanjowu usang'ambike.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkanjowo ukhala ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo pakhale chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo polowa mutu pakhale pakati pace; pakhale mkawo pozungulira polowa pace, wa nchito yoomba, ngati polowa pa malaya ociniiriza, pangang'ambike.