Exodus 28:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa mpendero wapansi wa mkanjowo, upange zinthu zonga makangaza. Zikhale za thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, kuzungulira mkanjo wonsewo. Pakati pa makangazawo pakhale timabelu tagolide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, upange mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira zokhala ndi maberu agolide pakati pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pa mbinyiru wace upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiirira, pambinyiru pace pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolidi pozungulira;