Exodus 28:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aroni azivala mkanjowo pamene akutumikira zaunsembe. Akamaloŵa m'malo opatulika pamaso pa Chauta kapena pochoka kumeneko, liwu la timabeluto lizidzamveka, kuti asafe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aroni auvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lake pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakutuluka iye, kuti asafe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aaroni azivala mkanjowo pamene akutumikira ngati wansembe. Kulira kwa maberu kuzimveka pamene akulowa mʼmalo opatulika pamaso pa Yehova ndiponso pamene akutuluka, kuti asafe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aroni aubvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lace pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakuturuka iye, kuti asafe.