Exodus 28:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Upangenso duŵa la golide wabwino kwambiri, ulembepo mozokota mau akuti, ‘Choperekedwa kwa Chauta.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Upange duwa lagolide wabwino kwambiri kukhala ngati chidindo ndipo uzokotepo mawu akuti, CHOPEREKEDWA KWA YEHOVA.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo upange golidi waphanthiphanthi woona, ndi kulocapo, monga malocedwe a cosindikizira. KUPATULIKIRA YEHOVA.