Exodus 28:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Likhaledi pamphumi pake pa Aroni, motero asenze iye yemwe cholakwa chilichonse cha pa zopereka zimene Aisraele amazipatulira Chauta. Kuti Chauta alandire zopereka za anthuzo, Aroni azivala duŵali pa nduŵira yake nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chizikhala pamphumi pake pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israele azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo chizikhala pamphumi pake kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lidzakhala pa mphumi ya Aaroni, motero iye adzasenza cholakwa chilichonse cha pa zopereka zilizonse zimene Aisraeli amazipatulira Yehova. Aaroni azivala chikwangwanichi pa mphumi pake nthawi zonse kuti Yehova alandire zopereka za anthu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cizikhala pamphumi pace pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israyeli azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo cizikhala pamphumi pace kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova.