Exodus 28:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ana a Aroni, uŵasokere miinjiro, malamba ndi nduŵira, kuti azisiyana ndi anthu ena, ndipo iwowo aziwoneka olemerera ndi olemekezeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo usokere ana a Aroni malaya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Upangirenso ana a Aaroni mwinjiro, malamba ndi nduwira kuti azioneka mwaulemu ndi molemekezeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo usokere ana a Aroni maraya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma.