Exodus 28:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Padzakhalenso lamba woluka mwaluso, womangira efodi, wolukira kumodzi ndi efodiyo. Lambayo nayenso adzakhale wa nsalu ya golide, ndi wa nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa chiombedwe chomwecho, ndi woombera kumodzi, wagolide, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lamba womangira efodi akhale wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Akhale wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa ciombedwe comweco, ndi woombera kumodzi, wagolidi, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.