Exodus 29:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muiphe, ndipo mutengeko magazi ake ndi kupaka pa khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa khutu la ku dzanja lamanja la ana ake aamuna. Upakenso pa chala chao chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja. Magazi ena uwaze pa mbali zonse za guwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake amuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo pa guwa la nsembe posungulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uyiphe ndipo utenge magazi ake ena ndi kupaka ndewere za makutu a kudzanja lamanja la Aaroni ndi ana ake aamuna. Upakenso pa zala zawo zazikulu za kudzanja lawo lamanja, ndi zala zazikulu za kuphazi lakudzanja lawo lamanja. Kenaka uwaze magazi otsalawo mbali zonse za guwalo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wace, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja la ana ace amuna, ndi pa cala cacikulu ca dzanja lao lamanja, ndi pa cala cacikulu ca phazi lao lamanja, ndi kuuwaza mwaziwo pa guwa la nsembe posungulira,