Exodus 29:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Utengeko magazi otsalira pa guwa ndiponso mafuta ena odzozera, uwaze Aroni ndi zovala zake. Uwazenso ana ake ndi zovala zao. Tsono iyeyo ndi ana ake adzakhala opatulika, pamodzi ndi zovala zomwezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo utapeko pamwazi uli pa guwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake amuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo utenge magazi ena amene ali pa guwa lansembe komanso pa mafuta ena odzozera ndipo uwawaze pa Aaroni ndi zovala zake ndi ana ake ndi zovala zawo. Ndiye kuti iyeyo ndi ana ake aamuna adzakhala opatulika pamodzi ndi zovala zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo utapeko pamwazi uli pa guwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zobvala zace, ndi pa ana ace amuna, ndi pa zobvala za ana ace amuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zobvala zace zomwe, ndi ana ace amuna ndi zobvala zao zomwe pamodzi ndi iye.