Exodus 29:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nkhosa yamphongo ija utengeko mafuta ake, mchira wake wamafuta, mafuta okuta matumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, imso ziŵiri ndi mafuta ozikutawo, ndiponso ntchafu ya ku dzanja lamanja, chifukwa nkhosa imeneyi ndi nsembe ya pa mwambo wodzozera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa nkhosa yayimuna ija utengepo mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake, ndiponso ntchafu yakumanja. Iyi ndi nkhosa ya mwambo wodzoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi me ira, ndi mafuta akukuta mat umbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;