Exodus 29:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Utenge nganga ya nkhosa yamphongo imene adaipha podzoza Aroni, ndipo uiweyule kuti ikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Imeneyi ndiyo idzakhala gawo lako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka utenge chidale cha nkhosa yayimuna imene inaperekedwa pamwambo wodzoza Aaroni, uchiweyule kuti chikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndipo chidzakhala gawo lako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.