Exodus 29:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake upatule zigawo za nkhosa yopereka pa mwambo wodzozera Aroni ndi ana ake, ndiye kuti nganga yoperekedwa ngati chopereka choweyula ija, ndiponso ntchafu yoperekedwa ngati chopereka choweyula ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake amuna;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uzipatule ziwalo zonse za nkhosa ya pa mwambo wodzoza Aaroni ndi ana ake. Chidale chimene unaweyula chija ndiponso ntchafu imene inaperekedwa ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo upatule nganga va nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; ziri za Aroni, ndi za ana ace amuna;