Exodus 29:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwana wa Aroni womloŵera m'malo kuti akhale wansembe, azidzavala zimenezi masiku asanu ndi aŵiri, pamene akuloŵa m'chihema chamsonkhano kukatumikira m'malo oyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mwana wake wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwake azivala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'chihema chokomanako kutumikira m'malo opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana amene adzalowa mʼmalo mwake monga wansembe pamene adzabwerera kudzalowa mu tenti ya msonkhano kudzatumikira ku malo wopatulika, adzavala zovala zimenezi masiku asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mwana wace wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwace azibvala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'cihema cokomanako kutumikira m'malo opatulika.