Exodus 29:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyama ikatsalako, kapena buledi akatsalako mpaka m'maŵa, utenthe. Asadye zimenezo chifukwa nzoyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza nchopatulika ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati nyama ina ya nkhosa ya pamwambo wodzoza ansembe kapena buledi zatsala mpaka mmawa, muziwotche, asazidye chifukwa ndi zopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza ncopatulika ici.