Exodus 29:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zonse zimene ndakulamulazi umchitire Aroni ndi ana ake aamuna omwe. Udzachite mwambo wakuŵapatula pa masiku asanu ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ake amuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uchitire Aaroni ndi ana ake aamuna zonse zimene ndakulamulazi. Uchite mwambo wowapatula kukhala ansembe masiku asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ace amuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri.