Exodus 29:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku ndi tsiku uzipereka ng'ombe yamphongo yopepesera machimo, kuti machimowo akhululukidwe. Uyeretse guwalo pakuliperekera nsembe yopepesera machimo. Kenaka ulidzoze kuti likhale lopatulika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yauchimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakuchita choteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lililonse uzipereka ngʼombe yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo kuti machimowo akhululukidwe. Ndiponso upatule guwalo popereka nsembe yopepesera ndi kulidzoza mafuta kuti likhale lopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yaucimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakucita coteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.