Exodus 29:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku asanu ndi aŵiri uzipereka nsembe zoyeretsera guwalo, ndipo uzilipatula. Pambuyo pake guwalo lidzakhala loyera kwathunthu, ndipo chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa masiku asanu ndi awiri uzipereka pa guwapo nsembe zoyeretsera guwalo, ukatero ndiye kuti uzilipatula. Ndipo guwa lansembelo lidzakhala loyera kwambiri, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza guwalo chidzayeretsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ucitire guwa la nsembe coteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo a guwa la nsembelo likhale lopatulikitsa; ciri conse cikhudza guwa la nsembelo cikhale copatulika.