Exodus 29:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono uzipereka mwanawankhosa wachiŵiriyo madzulo ndithu. Pamodzi ndi mwanawankhosayo, uziperekanso chopereka chachakudya ndi cha chakumwa, monga zam'maŵa zija, kuti zipereke fungo lokoma ndipo zikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira nsembe yaufa cha m'mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Upereke mwana wankhosa winayo madzulo pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa kuti ikhale fungo lokoma la chopereka chachakudya kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mwana wa nkhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unacitira copereka ca m'mawa ndi nsembe yace yothira, akhale pfungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.