Exodus 29:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono utenge zovala zija ndi kumuveka Aroni mwinjiro ndi mkanjo wautali wovala pamwamba pa efodi, ndiponso chovala chapachifuwa. Ndipo umange lamba woluka mwaluso uja m'chiwuno mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m'chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tenga zovala ndipo umuveke Aaroni mwinjiro, mkanjo wa efodi, efodiyo ndi chovala chapachifuwa. Umumange mʼchiwuno lamba wa efodi wolukidwa mwaluso uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo utenge zobvalazo ndi kubveka Aroni maraya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi capacifuwa, ndi kummangira m'cuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;