Exodus 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adayankha kuti, “Tsono ine ndikapita kwa Aisraelewo kukaŵauza kuti Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu, iwowo akakandifunsa kuti, ‘Dzina lake ndani?’ Ndiye ineyo ndikaŵauze chiyani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israele, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nao chiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lace ndani? ndikanena nao ciani?