Exodus 3:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pita ukaŵasonkhanitse atsogoleri onse a Aisraele, ukaŵauze kuti, Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, adandiwonekera; adandilamula kuti ndikuuzeni kuti wabwera kwa inu, ndipo zonse zimene akukuchitani Aejipito, waziwona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani m'Ejipito;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pita, ukawasonkhanitse akuluakulu a Israeli ndipo ukati kwa iwo, ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, anandionekera ndipo akuti Iye wadzakuyenderani ndipo waona mmene Aigupto akukuzunzirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muka, nukasonkhanitse akuru a Israyeli, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, ndi kuti; Ndakuzondani ndithu, ndi kuona comwe akucitirani m'Aigupto;