Exodus 3:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu watsimikiza kuti adzakutulutsani ku Ejipito kuno kumene mukuzunzika, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Dzikolo ndi lamwanaalirenji.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho wanenetsa kuti adzakutulutsani mʼdziko la Igupto, dziko la masautsoli kupita ku dziko la Akanaani, Ahiti, Aamori Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukuturutsani m'mazunzo a Aigupto, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.