Exodus 3:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adapitirira kunena kuti, “Zimene ukaŵauzezo, adzamva. Ndiye mukapite kwa mfumu ya ku Ejipito, iwe ndi atsogoleri a Aisraelewo, ndipo mfumuyo mukaiwuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, adakumana nafe. Tsono tikukupemphani, mutilole kuti tipite ulendo wa masiku atatu ku chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Akuluakulu a Israeli akakumvera. Kenaka iwe ndi akuluakuluwo mukapite kwa mfumu ya Igupto ndipo mukanene kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri, wakumana nafe. Tsono tikukupemphani kuti mutilole tipite pa ulendo wa masiku atatu mʼchipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzamveca mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akuru a Israyeli, kwa mfumu ya Aigupto, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'cipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.