Exodus 3:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo wa Chauta adamuwonekera ngati malaŵi a moto umene unkayaka m'chitsamba. Mose atapenya, adaona kuti chitsamba chili moto laŵilaŵi, koma osapsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera m'chilangali chamoto chotuluka m'kati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, chitsamba chilikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumeneko mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye mʼmalawi amoto mʼchitsamba. Mose anaona kuti ngakhale chitsambacho chimayaka koma sichimanyeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthenga wa Molungu anamuonekera m'cirangali camoto coturuka m'kati mwa citsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, citsamba cirikuyaka moto, koma cosanyeka citsambaco.