Exodus 3:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ine ndidzagwiritsa ntchito mphamvu zanga ndipo ndidzalanga Ejipito ndi zozizwitsa zomwe ndidzachite kumeneko. Zikadzachitika zimenezo, adzakulolani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aejipito ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aigupto ndi zozizwa zanga zonse ndizicita pakati pace; ndi pambuyo pace adzakulolani kumuka.