Exodus 3:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aejipito ndidzaŵafeŵetsa mtima pa anthu anga, kotero kuti pamene muzidzachoka, simudzapita chimanjamanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Ejipito; ndipo kudzakhala, pamene mutuluka simudzatuluka opanda kanthu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo ine ndidzafewetsa mtima wa Aigupto pa anthu anga, kotero kuti mukadzatuluka simudzapita wopanda kanthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Aigupto; ndipo kudzakhala, pamene muturuka simudzaturuka opanda kanthu;