Exodus 3:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi aliyense adzapempha Mwejipito woyandikana naye ndiponso amene amakhala naye m'nyumba, kuti ampatse zinthu zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Zimenezi mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi, motero mudzaŵalanda zonse Aejipitowo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mkazi yense adzafunse mnzake, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwake, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolide, ndi zovala; ndipo mudzaveke nazo ana anu aamuna ndi aakazi; ndipo mudzafunkhe za Aejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkazi aliyense adzapemphe Mwigupto woyandikana naye ndiponso mkazi amene akukhala mʼnyumba yake, kuti amupatse ziwiya za siliva ndi golide ndiponso zovala zimene mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi. Ndipo potero mudzawalanda zonse Aiguptowo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mkazi yense adzafunse mnzace, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwace, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolidi, ndi zobvala; ndipo mudzabveke nazo ana anu amuna ndi akazi; ndipo mudzafunkhe za Aaigupto.