Exodus 3:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapitirira kunena kuti, “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe.” Pompo Mose adadziphimba kumaso chifukwa adaopa kupenya Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.” Atamva zimenezi, Mose anaphimba nkhope yake chifukwa anaopa kuona Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ananenanso Ine ndine Mulungu wa atate wako, Molungu wa Abrahamu, Molungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yace; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu,