Exodus 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Chauta adati, “Ndaona m'mene anthu anga akuzunzikira ku Ejipito. Ndamva kulira kwao kofuna chithandizo, chifukwa cha anthu amene akuŵapsinja. Ndikudziŵa bwino kuzunzika kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m'Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati, “Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo chifukwa cha anthu amene akuwapsinja, ndipo ndakhudzidwa ndi masautso awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m'Aigupto, ndamvanso kulira kwao cifukwa ca akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;