Exodus 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndabwera kuti ndiŵapulumutse kwa Aejipito ndi kuŵatulutsa m'dziko limenelo, kuti ndikaŵaloŵetse m'dziko lalikulu lachonde. Dziko limenelo ndi lamwanaalirenji. Amene akukhala m'dziko limenelo ndi Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse mʼdzanja la Aigupto, kuwatulutsa mʼdzikolo ndi kukawalowetsa mʼdziko labwino ndi lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi, kwawo kwa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Aigupto, ndi kuwatumtsa m'dziko lila akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikuru, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.