Exodus 30:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ukamachita kalembera wa ana aamuna a Aisraele, munthu aliyense adzapereke kwa Chauta choombolera moyo wake, kuti mliri uliwonse usadzamugwere pamene kalemberayo akuchitika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene ukuchita kalembera wa Aisraeli, munthu aliyense ayenera kupereka kwa Yehova chowombolera moyo wake pamene akuwerengedwa. Motero mliri sudzabwera pa iwo pamene ukuwawerenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene uwerenga ana a Israyeli, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova ciombolo ca pa moyo wace, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.