Exodus 30:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense woyenera kulembedwa m'kalemberamo adzapereke theka la sekeli, ndiye kuti ndalama zolemera ngati magaramu asanu ndi limodzi, kutsata muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu (paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi aŵiri). Ndalama zimenezi zidzakhala zopereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi ndi zimene aliyense wolembedwa mu kawundula ayenera kupereka: theka la sekeli, kutanthauza ndalama zolemera magalamu asanu ndi limodzi malingana ndi kawerengedwe ka ndalama za ku Nyumba ya Mulungu. Paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi awiri. Theka la sekeli chidzakhala chopereka cha kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ici acipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo copereka ca Yehova.