Exodus 30:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndalama zoombolerazo zochokera kwa Aisraele, mudzagwiritse ntchito ya m'chihema chamsonkhano. Zidzakumbutsa Chauta za Aisraele, ndipo zidzakhala zoombolera moyo wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ulandire ndalama zopepeserazo kuchokera kwa Aisraeli ndipo zigwiritsidwe ntchito ya ku tenti ya msonkhano. Zoperekazi zidzakhala chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova, ndiponso zowombolera miyoyo yanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uzilandira ndarama za coteteza kwa ana a Israyeli, ndi kuzipereka pa nchito ya cihema cokomanako; kuti zikhale cikumbutso ca ana a Israyeli pamaso pa Yehova, kucita coteteza ca miyoyo yanu.