Exodus 30:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Utenge zonunkhira bwino kwambiri zokwanira makilogaramu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogaramu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa kinamoni, makilogaramu atatu a nzimbe zonunkhira bwino,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Utenge zonunkhira bwino kwambiri izi: makilogalamu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogalamu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa sinamoni, makilogalamu atatu a nzimbe yonunkhira bwino kwambiri,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu, ndi kinimani lonunkhira limodzi mwa magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi kane lonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,