Exodus 30:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono zonsezi udzapangire mafuta odzozera. Udzaziphatikize pamodzi monga momwe amachitira munthu wopanga zonunkhira. Mafuta amenewo adzakhale mafuta oyera, odzozera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa machitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ugwiritse ntchito zinthu zimenezi kupanga mafuta opatulika odzozera, mafuta onunkhira, apangidwe ndi mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa. Awa adzakhala mafuta opatulika odzozera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa macitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika.