Exodus 30:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musadzadzozere anthu wamba, ndipo musadzapangenso mafuta ena ofanafana nawo. Ameneŵa ngoyera ndipo kwa inu adzakhalabe oyera ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ake; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musadzadzozere munthu wamba mafuta amenewa, ndipo musadzapange mafuta wofanana ndi amenewa. Mafutawa ndi wopatulika ndipo akhale woyera kwa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ace; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.