Exodus 30:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense amene adzapange mafuta ena ofanafana nawo, kapena kudzozera munthu aliyense amene sali wansembe, adzamchotsa pakati pa anthu anzake.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wina aliyense amene adzapanga mafuta wonunkhira wofanana nawo kapena kudzozera mafutawa munthu wamba osati wansembe ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ali yense amene akonza ena otere, kapena ali yense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wace.