Exodus 30:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Upere gawo lina mosalala kwambiri, ndipo utatapako pang'ono, uike patsogolo pa bokosi lachipangano m'chihema chamsonkhano chokumanirako ndi anthu anga. Lubani ameneyu kwa inu akhale woyera kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Upere gawo lina mosalala kwambiri ndipo utapepo pangʼono ndi kuyika patsogolo pa Bokosi la Chipangano mu tenti ya msonkhano, kumene ine ndidzakumane nawe. Lubani ameneyu kwa inu adzakhala wopatulika kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nupere cina cisalale, nuciike cakuno ca mboni m'cihema cokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uciyese copatulika ndithu.