Exodus 30:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paguwapo usafukizepo lubani wosaloledwa, kapena zopereka za nyama yopsereza kapena za zakudya. Usadzaperekenso pamenepo chopereka cha chakumwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musafukizapo chofukiza chachilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa; musathirepo nsembe yothira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa guwapo usafukize lubani wachilendo kapena kuperekapo nsembe yopsereza kapena nsembe yaufa. Usathire pa guwapo ngakhale nsembe yachakumwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musafukizapo cofukiza cacilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena copereka; musathirepo nsembe yothira.