Exodus 31:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uza Aisraele kuti, ‘Muzisunga Sabata, tsiku langa lopumula, chifukwa ndilo chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi inu ndi zidzukulu zanu, choonetsa kuti Ine ndine Chauta, amene ndimakuyeretsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uza ana a Israeli kuti azisunga Masabata anga. Ichi chidzakhala chizindikiro pakati pa inu ndi Ine pamodzi ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo, chosonyeza kuti Ine ndine amene ndimakuyeretsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwe, lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo cizindikilo pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.