Exodus 31:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero muzisunga tsiku la Sabata, chifukwa ndi loyera kwa inu. Munthu aliyense wosalisunga, aphedwe. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo adzachotsedwe pakati pa anthu anzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira ntchito m'mwemo, munthu ameneyo asadzidwe mwa anthu a mtundu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Motero muzisunga tsiku la Sabata chifukwa ndi loyera kwa inu. Aliyense amene adetsa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; ali yense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti ali yense wakugwira nchito m'mwemo, munthu ameneyo asadzidwe mwa anthu a mtundu wace.