Exodus 31:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu agwire ntchito zake zonse pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku la Sabata lopumula, tsiku loyera la Chauta. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limeneli aphedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mugwire ntchito kwa masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, lopuma, tsiku lopatulika la Yehova. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Agwire nchito masiku asanu ndi limodzi; koma lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; ali yense wogwira nchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.