Exodus 32:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ataona kuti Mose wakhalitsako kuphiri osatsikako, adasonkhana kwa Aroni, ndipo adamuuza kuti, “Tiyeni mutipangire milungu yotitsogolera ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamugwera Moseyo, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito kuja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ataona kuti Mose akuchedwa kutsika mʼphiri, anasonkhana kwa Aaroni ndipo anati, “Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene anaona kuti Mose anacedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.