Exodus 32:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi mukufuna kuti Aejipitowo azidzanena kuti, ‘Adaŵatulutsa ku Ejipito ndi cholinga choipa choti akaŵaphere ku mapiri ndi kuŵaonongeratu pa dziko lapansi?’ Ukali wanu woyaka ngati motowo ubwezeni, ndipo musaŵaononge anthu anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi mukufuna kuti Aigupto azinena kuti, ‘Munali ndi cholinga choyipa chofuna kuwaphera ku mapiri kuno ndi kuwawonongeratu pa dziko lapansi pamene munkawatulutsa ku Igupto kuja?’ Ayi, chonde mkwiyo wanu woyaka ngati motowu ubwezeni ndipo sinthani maganizo ofunira zoyipa anthu anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akaneneranji Aaigupto; ndi kuti, Anawaturutsa coipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani coipaco ca pa anthu anu.