Exodus 32:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbukirani atumiki anu aja Abrahamu, Isaki ndi Israele ndiponso zija mudaŵalonjezazi molumbira pa dzina lanu, pamene mudaŵauza kuti, ‘Ndidzakupatsani zidzukulu zambiri, zochuluka ngati nyenyezi zakuthambo. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonse limene ndidalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lao mpaka muyaya.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, ‘Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumbukilani Abrahamu, Isake ndi Israyeli, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzichula nokha, amene munanena nao, Ndidzacurukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale colowa cao nthawi zonse.