Exodus 32:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose atafika pafupi ndi mahema aja, ndi kuwona mwanawang'ombe uja ndi anthu ovina, adakalipa kwambiri. Adaponya pansi miyala inali m'manja mwake ija, naiphwanya patsinde pa phiri paja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose atayandikira msasa ndi kuona mwana wangʼombe ndiponso kuvina, anakwiya kwambiri ndipo anaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwake, ndi kuyiphwanya pa tsinde la phiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pamene anayandikiza cigono, anaona mwana wa ng'ombeyo ndi kubvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwace, nawaswa m'tsinde mwa phiri.