Exodus 32:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo adakatenga mwanawang'ombe amene Aroni adapanga, namperapera ngati ufa, ndipo adakamtaya m'madzi. Tsono Aisraele aja adaŵamwetsa madziwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenga mwanawang'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye anatenga mwana wangʼombe amene anthu anapanga uja ndi kumuwotcha pa moto ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi. Kenaka anawaza fumbilo mʼmadzi ndi kuwamwetsa Aisraeli madziwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenga mwana wa ng'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israyeli.